Ntchito yofufuza ndege ya MH370 ya mdziko la Malaysia yomwe inasowa zaka zitatu zapitazo ati ayamba ayiyimitsa.
Malinga ndi malipoti a wailesi ya BBC, mayiko a Australia, Malaysia komanso China aganiza zoyimitsa ntchitoyi atakhumudwa kaamba koti ngakhale afufuza dera lalikulu mu nyanja ya mchere ya Indian akuti sizidaphule kanthu.
Mayikowa ati akukhulupilira kuti apeza mauthenga okwanira amene azathandize kupeza ndegeyi mtsogolo muno.
Ndege ya MH370 inasowa m’chaka cha 2014 pamene imachoka pa bwalo la ndege la Kuala Lumpur mdziko la Malaysia kupita ku Beijing.
Malipoti a mchaka cha 2016 ati akusonyeza kuti ndegeyi inagwera mu nyanja ya mchere ya Indian.