Anthu okhala mdera la mfumu yayikulu Bvumbwe m’boma la Thyolo awapempha kuti apitirize kugwirana manja ndi apolisi pa ntchito yolimbikitsa chitetezo cha ku madera.
Mkulu wa apolisi ya m’delari a Zecharia Mnkhambo ndi amene wanena izi m’dera la mfumu-yi pa mwambo wowunikira momwe apolisi agwilira ntchito zawo mchaka changothachi cha 2016 ndi kukonza mapulani a ntchito-zi mchaka cha 2017.
A Mnkhambo ati ngakhale kuti apolisi a m’derali agwira bwino ntchito zawo mchaka changothachi komabe akhala akukomana ndi mavuto ena pa ntchito zawo.
Polankhulanso m’modzi mwa akulu-akulu wowona za ubale wa pakati pa apolisi ndi anthu aku madera pogwira ntchito za chitetezo mdelaro a Billy Masoakutali anayamira ubale wabwino umene ulipo pakati pa apolisi ndi anthu a m’delaro.
Ena mwa anthu omwe anafika ku msonkhano-wu anali a zamalonda, mafumu , ogwira ntchito ku ndende ndi ena ambiri.