Mtsogoleri wakale wa dziko la Gambia, Yahya Jammeh wachoka mdzikolo atavomereza kugonja kwake pa chisankho atalamulira dzikolo kwa zaka 22.
Malipoti a wailesi ya BBC ati Jammeh pakadali pano ali mdziko la Guinea ndipo kenaka apita mdziko la Equatorial Guinea komwe amulamula kuti akakhale.
A Adama Barrow ndi omwe anapambana pa chisankho chomwe chinachitika m’mwezi wa December chaka chatha koma a Jammeh amatsutsana ndi zotsatirazi.
A Barrow ali mdziko la Senegal komwe analumbilitsidwa ngati mtsogoleri wa dziko la Gambia pamene a Jammeh amakana kutula pansi udindo wawo koma tsopano a Barrow ati abwerera mdziko lawo posachedwapa.
A Barrow ati akufuna kuti chilungamo chibwere poyera ndipo akhazikitsa komiti yapadera yomwe ifufuze maufulu a anthu omwe aphwanyidwa mu ulamuliro wa a Jammeh.
Malipoti ati asilikali a mmaiko a kuzambwe kwa Africa omwe anali mdzikolo potetezera a Barrow abwelera kwawo koma ena atsala pofuna kuwonetsetsa kuti chitetezo chilli mchimake.