Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Papa Apempha Akhristu Alimbikitse Umodzi, Apemphelera Okhudzidwa Ndi Zivomerezi

$
0
0

Mtsogoleri wa mpingo wa katolika pa dziko lonse papa Francisco wapempha akhristu kuti agwirane manja popemphelera umodzi  pakati pawo.

Malinga ndi malipoti a wailesi ya Vatican ati papa wanena izi pamene akhristu pa dziko lonse ali pakati pa sabata ya mapemphero a umodzi wa akhristu.

Papa atsekera mapempherowa lachitatu ndi mwambo womwe uchitike ku Vatican.

Iye wapempha akhristu akuti alimbike kupemphera kuti akwaniritse khumbo la umodzi pakati pawo.

Mwapadera papa wachita mapemphero opemphelera anthu omwe anakhudzidwa ndi zivomerezi zingapo zomwe zinachitika mchigawo cha pakati mdziko la Italy.

Iye wati ali nawo limodzi mmapemphero mabanja amene okondedwa awo anakhudzidwa ndi zivomerezi zi.

Papa walimbikitsanso onse omwe akugwira ntchito yopereka chithandizo kwa anthuwa kuti apitirize kutero.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Trending Articles


Mdima unadetsa dziko



<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>