Ndalama zoposa 11 million za America akuti zasowa mdziko la Gambia kutsatira kuchoka kwa mtsogoleri wa kale wa dzikolo a Yahya Jammeh.
Malipoti a wailesi ya BBC ati pali chisonyezo chakuti a Jammeh aba ndalamazi pamene amatuluka mdzikolo.
Anthu ati anawona galimoto komanso katundu wina akukwezedwa mu ndege usiku wa tsiku limene a Jammeh anatuluka mdzikomo.
A Yahya Jammeh anachoka mdzikolo loweruka atalamulira dzikolo kwa zaka 22 ndipo malipoti akusonyeza kuti athawira mdziko la Equatorial Guinea.
Iwo atuluka mdziko la Gambia atavomera kugonja kwawo pa chisankho chomwe chinachitika pa 1 December chaka chatha chomwe amakana kuvomereza zotsatira zake ponena kuti zinali ndi zovuta zina.
Mtsogoleri watsopano wa dzikolo a Adama Barrow adakali mdziko lo Senegal ndipo sizikudziwika kuti abwerera liti mdziko la Gambia.