Ntchito za pachipatala cha Ntcheu akuti zasokonekera kaamba ka ngozi ya moto umene wasakaza nyumba ndi zina pa chipatalachi.
Wofalitsa nkhani za pa chipatala-chi mayi Stella Kawalala ati akukhulupilira kuti ngozi-yi yomwe yachitika m‘mawa wa pa 3 mwezi uno, inachitika kaamba ka vuto la magetsi pa chipatalachi.
Padakalipano mkulu wa ku ofesi ya za umoyo pa chipatalachi Dr. Mike Chisema,wauza atolankhani a MANAkuti ngoziyi sinakhudze makhwala a pa chipatalachi.
Padakalipano ntchito yowonkhetsa ndi kufuna kudziwa mulingo wa katundu amene wasakazika pangoziyi akuti ili mkati.