Mtsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Francisco walimbikitsa anthu kuti akhale ndi kuthekera kwabwino kopereka mauthenga ndi cholinga chofuna kuti dziko lonse liziyenda mu chowona komanso mchikhulupiliro.
Papa walankhula izi kudzera mu uthenga wa tsiku loganizira zofalitsa mauthenga womwe likulu la mpingo wa katolika ku Vatican mu mzinda wa Rome latulutsa.
Mu uthengawu Papa wati magulu ogwira ntchito yofalitsa mauthenga akuyenera kuchotsa maganizo akuti nkhani zabwino siziyenda malonda, koma nkhani za kuzunzika kwa anthu mu njira zosiyanasiyana zomwe nthawi zina zimasanduka ngati za msangulutso.
Pamenepa Papa wati anthu akuyenera azipereka ma uthenga mwanzeru osati molimbikitsa zoyipa, koma azibweretsa zotsatira zabwino pa mavuto omwe alipo.
Uthengawu omwe mutu wake ndi “Usawope ndili Nawe, Kufalitsa uthenga wa chiyembekezo ndi chikhulupiliro watulutsidwa lachiwiri tsiku lomwe mpingo wakatolika umakumbukira Francis De Sales Woyera yemwe ndi nkhoswe ya atolankhani.