Bungwe laMalawi Red Cross Societylapempha mabungwe omwe siaboma kuti azilumikizana pomwe akugwira ntchito zosiyanasiyana zokhudza ngozi zogwa mwadzidzi.
Mkulu wa bungweli m’boma la Zomba, aBlessings Mlowokandi omwe anena izi, pomwe bungweli limafotokozera mabungwe-wa m’bomalo za ubwino wogwira ntchitolimodzi.
A Mlowoka ati kugwilira ntchito limodzi maka mu nthawi ya mavuto ogwa mwadzidzi kumathandiza kuchepetsa ntchito ndi zipangizo zogwilira ntchitoyi.