Arki episikopi wa Arki dayosizi ya Lilongwe Ambuye Tarcisius Ziyaye asankha gulu la akhristu oposa 75 omwe athandize pozokonzekera zansonkhano wa bungwe la aepiskopi la Association of Member Episcopal Conferences of Eastern and Central Africa [AMECEA].
Msonkhanowo omwe uzabweretse pamodzi nthumwi zoposa 300 kuphatikizapo ma Kadinala, ma Arki episkopi ndi ma Episkopi ochokera m’mayiko ambungweli uzachitikira ku Malawi kuyambira pa 14 mpaka pa 26 July, 2014 mumzinda wa Lilongwe.
Polankhula pa msonkhano womwe anachita ndi akhristu omwe asankhidwa kuchokera mmaparishi osiyanasiyana mu Arki dayosizi ya Lilongwe potengera ndi maluso awo, Ambuye Ziyaye anayamikira akhristuwo chifukwa chofika mwaunyinji.
“Ngakhale uthenga wokuyitanani ku msonkhano uno munawulandira mochedwa ndakondwera kuti mwafika mwaunyinji zomwe zikusonyeza kuti mumawukonda mpingo wanu ndipo zimenezi zikupereka chiyembekezo choti msonkhano wa AMECEA uzakhala wopambana,” anatero Ambuye Ziyaye.
Ambuye Ziyaye anatsimikiziranso akhristuwo kuti ‘’Kugwira ntchito za mpingo ndi mtima wonse ndi chinthu chofunikira kwambiri ndipo pamene mukudzipereka pa ntchito ngati zimenezi dziwani kuti Mulungu sangakusiyeni osakudalitsani.”
Gulu latsopano la akhristuwa liphatikizana ndi gulu lina la akhristu oposa 20 omwe akhala akuyendetsa zokonzekera za msonkhano wa AMECEA kuchokera mchaka cha 2012 maka kumbali yotolera ndalama komanso kufalitsa za msonkhanowu. Gulu latsopano la akhristuwa lagawidwa kuti litumikire m’ma komiti owona za chakudya, zofalitsa nkhani, za malo ogona, chitetedzo, umoyo komanso ya dongosolo.
Malinga ndi wapampando wa komiti yayikulu yowona zokonzekera msonkhano wa AMECEA a Peter Kulemeka pa 26 April, 2014 kuzakhala mwambo womwe maanja atatu azabwereze malumbiro awo a ukwati ngati njira imodzi yofuna kutolera ndalama za msonkhanowu. Malinga ndi a Kulemeka mwambo wa msembe ya misa uzachitikira pa parishi ya St. Patricks ku Area 18 ndipo pambuyo pake pazakhala mwambo waukulu ku Bingu International Conference Centre.