Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

DAYOSIZI YA MANGOCHI IKUZINDIKIRITSA ACHINYAMATA ZOPEWA ZIWAWA

$
0
0

Pamene kwangotsala sabata zowerengeka kuti anthu adzaponye voti pa chisankho cha patatu pa 20 May, Dayosizi ya Mangochi yampingo wakatolika yati ikudzipereka powonetsetsa kuti chisankhochi chidzachitike mwa bata ndi mtendere.

Mkulu wa mu ofesi yofalitsa nkhani mu Dayosizi ya Mangochi bambo Raphael Mkuzi anena izi lolemba pamene Dayosiziyi yayamba kugwiritsa ntchito miyambo ya misa pozindikiritsa anthu maka achinyamata za kuipa kotenga mbali pa ziwawa.

‘’Ife ngati mpingo timakhulupirira kuti munthu ndi thupi ndi mzimu pamodzi ndie kumbali ya ndale kwenikweni timakhudza ku moyo wa thupi,’’ ayankhula motero bambo Mkuzi.

Bambo Mkuzi ati kudzera m’mabungwe osiyanasiyana a mpingowu ukuchitanso chotheka kuti anthu adziwe zoyenera kuchita pokonzekera chisankhochi.

‘’Tili ndi nthambi zathu zimene timazigwiritsa ntchito monga bungwe la chilungamo ndi mtendere la CCJP lomwe pakali pano lili kalikiliki kuphunzitsa anthu za mmene angayendetsere bwino kampani yawo komanso mmene angakhalire bwino pa nthawi yokonzekera chisankho chapatatuchi,’’ atero Bambo Mkuzi omwenso ndi mlembi wowona za utumiki mu Dayosizi ya Mangochi.

Dayosiziyi yadzudzulanso zomwe zidachitika kwa Goliati m’boma la Thyolo pamene anthu awiri adaphedwa pa ziwawa zomwe zidabuka pa msonkhano wa chipani cholamula cha Peoples.

‘’Tinene momveka pano kuti ife ngati mpingo takhumudwa ndi zomwe zayamba kuwoneka kale kuti anthu ayamba kumamenyana, kukhapana komanso kuphana chifukwa chonena kuti akulimbikitsa za chipani chawo kuti chizapambane. Zimenezi sizikuyenera kuchitika. Mpingo umafuna kuti anthu akhale ndi utsogoleri wabwino ndipo sitimayang’ana za chipani.’’ Atero Bambo Mkuzi.

Bambo Mkuzi ati ndikofunika kuti achinyamata asagwiritsidwe ntchito ndi andale poyambitsa ziwawa.

‘’Tikulimbikitsa ndi kupempha achinyamata maka maka amene amagwiritsidwa ntchito nthawi zambiri ndi anthu andale kuti nthawi ino ya kampeni apewe kugwiritsidwa ntchito ndi anthu amene angofuna kuti athandizidwe lero mawa azawataye,’’ anatsiriza motero Bambo Mkuzi.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Trending Articles


Mdima unadetsa dziko



<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>