Anthu okhala mdera lozungulira nyanja ya Chirwa m’boma la Zomba ati ali pa mavuto a njala ya dzawoneneni kutsatira kuphwera kwa nyanja ya Chilwa.
Mfumu Njala ya kwa Sub T/A Nkagula m’bomalo yauza Radio Maria Malawi kuti anthu a mderali alinso pa umphawi kaamba koti usodzi ukukanika chifukwa cha kuphwera kwa nyanjayi.
Iwo apempha anthu okhala madera ozungulira nyanjayi kuti aleke kulima ndi kudula mitengo m’mbali mwa nyanjayi komanso mitsinje kaamba koti ati ndi zimene zachititsa kuti nyanjayi iphwere.
Pamenepa mfumu Njala yapempha boma kuti lithandize anthuwa ndi chakudya mwansanga.
Polankhulapo m’modzi mwa ochita malonda ogulitsa nsomba mai Stevina Chitedze ati pakadalipano asodzi omwe amapha nsomba munyanjayi akukhala moyo ovutika popeza sakuphaso nsomba.