Wolemba nkhani zamasewero ku Radio Maria Malawi Foster Mkwamba wakhala m’modzi mwa atolankhani omwe achita bwino polemba nkhani za masewero mu mpikisano wa FIFA/FAM Under 20, mchaka cha 2017.
Mkwamba yemwe wakhala pa nambala 2 kutsatira Sam Banda wa wayilesi ya Blantyre Synod wati zonsezi zachitika kaamba kakulimbikira kwake. Iye wapempha anthu mziko muno kuti asamaonere pansi Radio Maria Malawi pa nkhani zamaswero.
Polankhulapo mkulu oyang’anira za mapologamu ku Radio Maria Malawi a Emmanuel Kaliati ati ndi okondwa kaamba ka zimene zachitikazi ndipo wailesiyi ili m’malingaliro oyambitsa pologalamu yapadera ya zamasewero.