Mtsogoleri wa chipani chotsutsa boma cha Umodzi, Professor John Chisi wati sakuwonapo vuto pa kuchulukana kwa zipani za ndale mdziko muno.
Professor Chisi wanena izi polankhula ndi Radio Maria Malawi. Iye wati ngakhale dziko lino litakhala ndi zipani mazanamazana koma chofunika kwambiri ndi choti zipanizo zibweretse mgwirizano pakati pa a Malawi mdziko muno.
Ndipo polankhulapo, m’modzi mwa ankhlakale pa ndale mdziko muno a Humphreys Mvula agwirizana ndi a Chisi pa nkhaniyi koma ati kuchuluka kwa zipani kumasokoneza ntchito za chitukuko mdziko.