Dziko la Ethiopia laletsa mchitidwe opereka ana kwa mzika za m’maiko ena, zomwe zimafika mdzikolo kufuna ana oti adzikawasamalira.
Ganizoli, ladza, boma litalandira malipoti oti ana otengedwa ndi anthuwa amazunzika m’manja mwa makolo awo atsopanowo.
Dzikolo, akuti ndi limodzi mwa maiko omwe amadaliridwa kwambiri ndi mzika za m’maiko ena, maka za ku America, zomwe zimafuna ana m’maiko ena pazifukwa zosiyanasiyana.
Malipoti a wailesi ya BBC akusonyeza kuti ana makumi awiri mwa ana 100 aliwonse, omwe amatengedwa ndi mzika za m’maiko ena padziko lonse, amachokera mdziko la Ethiopia-lo.