Mkulu wa ma Jaji Justice Anastanzia Msosa wayamikira bungwe la Catholic Commission for Justice and Peace [CCJP]mu Arki dayosizi ya Lilongwe chifukwa chokhazikitsa pulojekiti yolimbikitsa kuti milandu ing’ono ing’ono isamathere ku mabwalo amilandu akuluakulu.
Justice Msosa wanena izi mumzinda wa Lilongwe lolemba sabata ino pamene bungweli limawunikira ntchito za mu pulojekitiyi kwa akulu akulu osiyanasiyana okhuzidwa.
Justice Msosa wati pulojekiti yolambalalitsa milandu ing’ono ing’ono ndiyothandiza kuti ndende za mdziko muno zisamakhale zozadza ndi anthu omwe apalamula milandu ing’ono ing’ono.
Mkulu wa bungwe la CCJP mu Arki dayosizi ya Lilongwe Peter Chinoko wati pulojekitiyi ikulimbikitsa kuti anthu omwe amapezeka ndi milandu ing’ono ing’ono azipatsidwa zilango zina kusiyana ndi kukagwira ukaidi.
‘’Ndi zomvetsa chisoni kuti ndende zathu ku Malawi ndi zozadza kwambiri. Mwachitsanzo ndende ya Maula inamangidwa kuti izikhala ndi anthu 800 koma kukukamba pano ku Maula kuli anthu oposa 2500,’’ watero Chinoko.
Chinoko wati mwa zina kudzera ku pulojekitiyi anthu omwe apalamula milandu amalamulidwa kuti abweze katundu wobedwayo.
‘’Mwachitsanzo wina waba nkhuku. Timadziwa kuti nkhuku ku Malawi kuno yokwera mtengo kwambiri siposa K4000 ndie kwa munthu yemwe waba nkhuku timamuuza kuti abweze ndipo akatero timamuuza kuti apite ku sukulu kuti akaphunzire za kuipa kwa kuba.’’ Watero Chinoko.
Bungwe la CCJP likugwira pulojekitiyi pamodzi ndi apolisi, azandende, a Legal Aid, aunduna wazachilungamo, ofesi ya mkulu wozenga milandu ya boma komanso a makhothi.