Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

A MALAWI SITIKUKHWIMA PA NDALE

$
0
0

Mtsogoleri wa mpingo wa Anglican mdziko muno Bishopu Brighton Vita Malasa ati ziwawa zomwe zinachitika pa 8 march kwa Goliati mboma la Thyolo zawonetsa poyera kuti anthu mdziko muno sakukhwima pa ndale.

Bishopu Malasa omwenso ndi Bishopu wa Dayosizi ya Upper Shire ya mpingo wa Anglican ndiye wanena izi ku Mpondasi mboma la Mangochi loweruka sabata yatha pomwe Dayosiziyi imathokoza Mulungu komanso kutsanzikana ndi Canon John Chilombe omwe akukatumikira mdziko la Zambia pamwambo omwe   Pulezidenti wadziko lino Dr Joyce Banda anali nawonso ngati mlendo wolemezeka.

Bishopu Malasa adati ndikofunika kuti atsogoleri azipani apewe kunyozana ndipo m’malo mwake apange kampeni yolongosolela anthu mfundo zawo.

‘’Ife ngati mpingo wa Anglican ndi wokhumudwa ndi ziwawa zomwe zinachitika kwa Goliati komwe mpaka anthu anataya miyoyo yawo. Ziwawa zomwe zikuchitikazi ndi chizindikiro choti Malawi ngati dziko sitikukhwima pa ndale. Masiku apitawa tinatulutsa chikalata chomwe ife tikudzudzula mchitidwe woyipa umenewu.’’Adatero Bishopu Malasa.

Pulezidenti Banda anavomerezana ndi mawu a Bishopu Malasa ndipo anati ndikofunika atsogoleri azipembedzo apempherere dziko lino kuti pakhale kampeni ya mtendere.

Poyankhula zokhudza Canon John Chilombe, Dr Joyce Banda anati Canon Chilombe ndi m’modzi mwa anthu omwe wawathandiza kwambiri powalangiza pa nkhani za uzimu.

Bishopu Robert Mumbi wa Dayosizi ya Luapula mdziko la Zambia komwe Canon Chilombe azikatumikira anayamikira mpingo wa Anglican mdziko muno chifukwa chotumiza wamsembeyu kukagwira ntchito za umishonale kunja kwa dziko lino.

Canon Chilombe ndi wamsembe  wachitatu  wa mpingo wa Anglican mdziko muno kukatumikirapo mdziko la Zambia ndipo ena ndi malemu Leonard Mwaungulu kuzanso Archbishopu opuma Bernard Malango omwe anakhalapo Bishop wa Dayosizi ya Northern Zambia kwa zaka 14.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Trending Articles


Mdima unadetsa dziko