M’tsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Francisco wafunira zabwino nthumwi zomwe zikuchita nawo msonkhano wa bungwe loona za kayendetsedwe kabwino ka chuma la World Economic Forum umene umachitikira ku Davos m’dziko la Switzerland.
Papa watumiza uthenga-wu kudzera kwa wapampando wa bungwe-li Professor Klaus S’kwabu ku msonkhanowo.
Iye wati akukhulupilira mfundo zomwe zimangidwe ku msonkhanowu zithandiza pa ntchito zokweza chuma cha mayiko padziko lonse.
Msonkhano-wu unayamba pa 23 January ndipo watha pa 26 January.
Nthumwi zochokera m’mayiko osiyanasiyana omwe ali mamembala wa bungwe-li ndi omwe achita nawo msonkhano-wu.