Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Anthu 100 Afa Mdziko la Afghanstan

$
0
0

Anthu oposera 1 hundred afa mu mzinda wa Kabul mdziko la Afghanstan kaamba ka mabomba omwe anaphulitsidwa mu mzindawu.

Malipoti a wailesi ya BBC ati anthu omwe achita chiwembuchi anayika mabombawa mu galimoto ya mtundu wa Ambulance ndipo anakayimitsa pa malo pamene pamapezeka anthu ambiri pomwe pali maofesi a boma la dzikolo ngakhalenso a akazembe mmaiko osiyanasiyana.

Padakali pano dziko la Afghanstan lakhazikitsa lero lamulungu kuti likhale lokhudza maliro a anthuwa komanso kuti achibale akhale akuyang’ana abale awo omwe avulala pa ngoziyi mzipatala za mu mzindawu.

Gulu la zauchifwamba la Taliban ati lavomera kuti ndi lomwe lachita chiwembuchi ndipo chachitika patatha sabata imodzi patachitikanso chiwembu china pomwe anthu 22 anaphedwa pa hotela ina mu mzinda womwewu wa Kabul.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>