Mtsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Francisco wauza bungwe lomwe limapereka thandizo kwa anthu omwe akumana ndi mavuto a njala,nkhondo, matenda ndi zina la Italian Red Cross kuti ntchito yomwe limagwira ndi yofunika pa dziko lonse.
Papa amalankhula izi loweruka ku likulu la mpingowu ku Vatican mu mzinda wa Rome pa mwambo wolandira anthu atsopano a m’bungweli okwana 7 sauzande. Pamenepa Papa wati bungweli lakhala likugwira ntchito yabwino mdziko la Italy ngakhalenso pa dziko lonse. Mtsogoleri wa mpingo wakatolikayu wati aliyense payekhapayekha akuyenera kuyamikira bungweli kaamba koti limakhala likugwira ntchito nyengo zovuta.