Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Anthu Omwe Akuthandizidwa ndi CADECOM Akhale Odziyimira Pawokha-Ambuye Stima

$
0
0

Episkopi wa dayosizi ya mpingo wa katolika ya Mangochi Ambuye Montfort Stima apempha anthu omwe akuthandizika ndi bungwe lowoona za chitukuko mu mpingowu la CADECOMkuti akhale odziyimira pawokha kudzera mu ntchito zomwe bungweli likugwira.

Ambuye Stima alankhula izi loweruka ku parishi ya Mpiri mu dayosiziyi pa mwambo wokhazikitsa ndondomeko ya masomphenya a chitukuko ya zaka za 2017mpaka 2022yomwe bungweli mu dayosiziyi likhale likugwiritsa ntchito.

Iwo ati pamene bungweli likugwira ntchito zofuna kutukula miyoyo ya anthu, anthu eni ake akuyenera kuchilimika ndi cholinga choti apindule ndi ntchitozi.

Pamenepa Ambuye Stima apemphanso anthuwa kuti alimbike pa nkhani ya ulimi pofuna kuti azikhala ndi chakudya chokwanira chaka chonse.

Polankhulapo yemwe anayimilira wapampando wa bungweli mu dayosiziyi a George Chimphonda ati mu ndondomekoyi muli mfundo zisanu ndi ziwiri zomwe bungweli likuyenera kukwaniritsa pofika chaka cha 2022.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>