Apolisi m’boma la Chikwawa akusunga m’chitokosi bambo wina wa zaka 20za kubadwa yemwe dzina lake ndi William Masiyamphuka, kaamba komuganizira kuti wagwilira m’sungwana wa zaka zisanu.
Padakalipano malipoti a Malawi News Agency(MANA) asonyezanso kuti a Eliya Shadreck omwe anapalamulanso mlandu ngati womwewu m’bomalo, bwalo la milandu lawapeza olakwa ndipo awalamula kuti akakhale kundende ndi kukagwira ntchito ya kalavula gaga kwa zaka khumi ndi ziwiri (12).
Malingana ndi wofalitsa nkhani za apolisi m’boma-lo, Foster Benjamin, boma la Chikwawa Lalandira milandu itatu yokhudza kugwililira m’mwezi wa January wokha chomwe ati ndi chiwerengero chokwera kwambiri poyerekeza ndi zaka zapitazo ndipo apempha makolo kuti azipereka chisamaliro chokwanira komanso kuyang’anira bwino ana awo.