Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Apezeka Atafa Podzimangilira

$
0
0

Bambo wina wa zaka 37 zakubabdwa wapezeka atafa pozimangilira kwa Chikanda mu mzinda wa Zomba.

Mneneri wa apolisi m’chigawo cha kummawa kwa dziko lino Inspector Joseph Sauka wauza Radio Maria Malawi kuti mkuluyu Alinafe Matope,wapezeka lero m’mawa atazimagilira pafupi ndi nyumba yake koma chifukwa chomwe wachitira izi sichikudziwika.

Malipoti a ku chipatala chachikulu cha Zomba asonyeza kuti mkuluyu wafa kaamba kobanika ndi chingwe chomwe anadzimanga nacho ndipo apolisi ati akufufuza kuti adziwe chomwe chachititsa mkuluyu kuti azimangilire.

Sauka wati ndi okhudzidwa ndi kuchuluka kwa imfa zodza kaamba kozimangilira zomwe zachuluka mchigawochi.

Alinafe Matope amachokera m’mudzi mwa Chikanda kwa mfumu yaikulu Chikowi m’boma lomwelo laZomba.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>