Mpingo wa katolika mdziko muno wapempha akhristu ake kuti asagule nsalu yomwe ikupezeka pa msika yomwe ikusonyeza mayina a Papa Franciscko, Benedict 16.
Mlembi wamkulu wa bungwe la ma episkopi a mpingo wa katolika mdziko muno la Episcopal Conference Of Malawi (ECM) bambo Henry Saindi auza Radio Maria Malawi kuti nsaluyi yomwe ikupereka chithunzithunzi choipa cha a papa ndi yosavomerezeka ndi mpingowu.
Iwo ati bungweli likuyembekezeka kukambirana ndi kampani yomwe yatulutsa nsaluyi kuti isapezekenso pa msika.