Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Papa Alimbikitsa Ubale wa Mpingo wa Katolika ndi Anglican

$
0
0

M’tsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse papa Francisco waonetsa chitsanzo cha ubale wabwino pakati pa mpingo wakatolika ndi wa Anglican.

Papa wachita izi atakayendera akhristu a mpingo wa Anglican ku Parish ya mpingo-wu ya All Saints yomwe ikupezeka mu mzinda wa Rome m’dziko la Italy.

Malingana malipoti a wailesi ya kulikulu la mpingo wakatolika ku Vatican, Papa Francisco akuti wachita izi ngati njira imodzi yokondwelanso limodzi ndi mpingo-wu pomwe ukuchita chaka, cha zaka mazana awiri (200) chikhadzikitsileni tchalichi loyamba la mpingo-wu umene maziko ake ali m’dziko la England.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>