Bwana-mkubwa wa boma la Mangochi a James Manyetera ayamikira sukulu ya ukachenjede ya DMI yomwe imayendetsedwa ndi amsembe a mpingo wakatolika mu chipani cha Missionaries of Mary Immaculate(MMI) kamba kolimbikitsa ophunzira kuchita nawo masewera osiyanasiyana.
A Manyetera alankhula izi pakutha pa mwambo wa tsiku la zamasewela pa sukulu-yi. Iwo ati zomwe sukuluyi ikuchita zikulingana ndi mapulani a boma pokweza nkhani za masewela m’dziko muno.
Polankhulanso bambo Sengol Jeyaslan amene amayimilira chipani cha Missionaries of Mary Immaculate poyendetsa ntchito za sukulu-yi ati sukulu-yi imakhulupilira kuti masewera ndi ofunika kwambiri pakati pa ophunzira chifukwa amavumbulutsa luso lachibadiwe lomwe ophunzirawa ali nalo zomwe zimathandiza pachitukuko cha dziko.
M’mau ake President wa bungwe loyimira ophunzira pa sukulu-yi Timothy Madalitso Ngwira wati ndi okondwa ndi momwe mwambo wa tsikuli wayendera ndipo ali ndi chikhulupiliro chakuti mwambowu uzikhala wopamba chaka ndi chaka.