Dziko la South Sudan lalengeza kuti mmadera ena a mdzikolo anthu akuvutika ndi njala.
Malinga ndi boma la dzikolo komanso bungwe lowona za mgwirizano wa maiko a pa dziko lonse la United Nations UNanthu 1 hundred sauzande ndi omwe akukumana ndi vutoli padakali pano ndipo ena 1 miliyoni akhala akukumananso ndi vutoli ngati sathandizidwa mwansanga.
Malipoti a wailesi ya BBC ati nkhondo ya pa chiweniweni yomwe yakhala ikuchitika mdzikolo komanso vuto la zachuma ndi zomwe zachititsa kuti dzikoli likumane ndi vutoli.
Maiko a Yemen, Somalia komanso dera lina la dziko la Nigeria ali pali chiopsezo chakuti atha kukumananso ndi vuto la njala koma dziko la South Sudan ndi loyamba kubwera poyera.