Bungwe lomenyera ma ufulu a anthu achikulire, la Malawi Network of Older People (MANEPO) lati atolankhani ndi ofunika pa ntchito yoteteza maufulu a anthu achikulire mdziko muno.
Mkulu wa bungweri a Andrew Kabvala anena izi mu mzinda wa Blantyre pa maphunziro a tsiku limozi omwe bungweri linakonzera atolankhani ndi cholinga chofuna kuwazindikiritsa udindo wawo polimbikitsa ntchito yoteteza maufulu omwe anthu achikulire ali nawo.
Iwo ati atolankhani ndi ofunika kwambiri maka pano pomwe anthu achikulire akukumana ndi mavuto osiyanasiyana monga kuchitiridwa nkhanza ndi zina zambiri.