Khonsolo ya boma la Balaka yapempha kuti pakhale ubale wabwino pakati pa adindo ndi makomiti a za chitukuko m’bomalo.
Bwanamkubwa wa bomalo, Rodrick Mateauma ndi yemwe wanena izi potsatira mphekesera yomwe yakhala ikumveka yoti magulu awiriwa sakulumikizana pa ntchito zachitukuko m’bomalo.
Iye watinso zikuonetsa kuti vuto lonseli likuchitika kaamba koti makhansala ena sakuzindikirabe udindo wawo ndi zoyenera kuchita izi ndi zimene zikuchitisa kuti makomiti achitukuko ndi makhansalawa adzisemphana pakagwiridwe ka ntchito.
Polankhulapo m’modzi mwa makhansala a m’bomalo Peterson Bwanali wathirirapo ndemanga kuti ubale wa magulu awiriwa wakhala usakuyenda bwino m’bomalo.