Matupi oposera 70 a anthu akufa akuti apezeka akuyandama kudera lina mu nyanya yayikulu ya Atlantic m’dziko la Lybia.
Akatswiri pa ntchito zopulumutsa anthu pa ngozi zochitika pamadzi akuti ndi amene atulutsa mitembo ya anthuwo munyanja-yi.
Pofotokozera atolankhani a wailesi ya BBC m’modzi mwa akuluakulu a bungwe la Red Cresent m’dzikomo wati padakalipano gwero la imfa ya anthu-wa silikudziwika kamba koti sanalandire malipoti a mtundu wina uli wonse okhudza ngozi ya pamadzi mu nyanja-yi.
Padakalipano ntchito yofufuza bwino gwero la imfa ya anthu-wo ili mkati.