Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Zuma Atula Pansi Udindo

$
0
0

Mtsogoleri wa dziko la South Africa, Jacob Zuma watula pansi udindo wake.

Malinga ndi malipoti a wailesi ya BBC, Zuma wati akuchoka pa udindowu mwa kufuna kwake osati kaamba kokakamizidwa ndi chipani chake cha African Bnational Congress (ANC).

Chipani cha ANC chinapempha Zuma kuti atule pansi udindo wake kupanda apo aphungu a kunyumba ya malamulo ndi omwe atamuchotse kudzera mu voti.

Mtsogoleriyu yemwe ndi wa zaka 75 wakhala akupemphedwa kuti atule pansi udindo ndi kupereka mpata kwa wachiwiri wake Cyril Ramaphosa amene anasankhidwa kukhala mtsogoleri watsopano wa chipani cholamulacho.

Zuma amene walamula dziko la South Africa kuyambira mchaka cha 2009, akukhudzidwa ndi nkhani za katangale zosiyanasiyana mdzikomo.

Iye wati waganiza zotula pansi udindo wake pofuna kudzetsa bata mu chipani chake cha ANC pomwe padakalipano muli mpungwepungwe komanso kugawikana.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>