Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Apha Msuweni Kaamba Kogona ndi Mkazi Wake

$
0
0

Apolisi m’boma la Mchinji amanga mamuna wina kaamba komuganizira kuti anapha msuweni wake atamugwira akuchita zadama ndi mkazi wake.

Malinga ndi wofalitsa nkhani za apolisi m’bomalo, Inpector Kaitano Lubrino, mwezi wa September chaka chatha achibale a malemuyu anakanena kupolisi za kusowa kwa Lebias Timoti, ndipo ntchito yomufunafuna malemuyu inayamba kufikira mwezi wa January chakachino pamene apolisi anagwira oganiziridwa-yu Ezala Kamwendo amene ndi msuweni wa malemuyu kudzera mu zokambirana zawo za mu lamya ya m’manja.

Mkuluyu ati anavomera kuti anapha msuweni wakeyu pomupotokola khosi ndikukamukwirira mu m’tsinje wa Liwuye, pamene anamugwira akuchita zadama ndi mkazi wake m’mudzi mwa Kuphazi m’dera la mfumu yayikulu Katsabola m’dziko la Mozambique.

Apolisi aku Malawi molumikizana ndi apolisi a mdziko la Mozambique anapita kumalo komwe anakamukwirirako ndipo anakapeza thupi la malemuyu mu mtsinjewo koma litawonongeka.

Ezala Kamwendo yemwe amachokera m’mudzi wa Mabvere kwa mfumu ya yaikulu Mabvere m’boma lomwelo la Mchinji akaonekera ku bwalo la milandu ndi kukayankha mlandu wakupha omwe ukutsutsana ndi gawo 209 la malamulo oyendetsera dziko lino.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>