Akiepiskopi wa Akidayosizi ya Lilongwe Ambuye Tarcisius Ziyaye athokoza mtsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Fransisko chifukwa chowapatsa Pallium yatsopano chomwe ndi chizindikiro chowonetsa kutumidwa ndi Papa. Pallium ndi chovala chokolekera chomwe Papa amachipereka kwa Akiepiskopi yemwe wamutumidwa kukatumikira mu Akidayosizi ina. Ambuye Ziyaye pamodzi ndi Akiepiskopi Thomas Luke Msusa, Akiepiskopi wa Akidayosizi ya Blantyre anali mgulu la ma Akiepiskopi a m’maiko osiyanasiyana omwe anapatsidwa Pallium yatsopano ndi mtsogoleri wampingo wakatolika pa dziko lonse Papa Fransisko pa mwambo womwe unachitikira mumzinda wa Vatican. Arkiepiskopi Msusa omwe anakhalapo episkopi wa dayosizi ya Zomba anakakhala nawo pa mwambo wolandira Pallium mwezi wa May mumzinda wa Vatican mdziko la Italy koma Ambuye Ziyaye analephera kupita ku mwambowo. Ambuye Ziyaye omwe poyamba anali Akiepiskopi wa Akidayosizi ya Blantyre analandira Pallium kudzera kwa nduna ya Papa m’maiko a Malawi ndi Zambia Akiepiskopi Julio Murrat pa mwambo wa msembe ya ukaristia wotsekulira msonkhano wa AMECEA. “Mwina ena titha kudabwa lero kuti kodi mmene ndinali ku Blantyre ndinalibe Pallium inapsa? Kapena inabedwa? Zakhala bwanji? A Papa akasamutsa Arkiepiskopi kumutuma kupita ku Arkidayosizi ina popeza kuti ndi udindo watsopano kumeneko amapereka Pallium” anatero Ambuye Ziyaye. Ambuye Ziyaye anati analephera kukalandira okha Pallium kuchokera kwa Papa Fransisko chifukwa chotanganidwa kwambiri. “Mwezi wa May ndimayendayenda mpaka June monga kupita ku Kenya kukapereka ma degree ku sukulu ya ukachenjede ya bungwe la AMECEA ndi ntchito zina. Ndinapempha kwa akulu anga kuti ndilandire Pallium lero ndie atandilola mchifukwa ndalandira pano.” Anatsiriza motero Ambuyewa omwenso ndi wapampando wa bungwe la AMECEA.