Komiti yomwe ikuyendetsa chikondwelero cha mayimbidwe cha Radio Maria Choir Festival chomwe chichitike loweruka pa 22 November yati zokonzekera zonse za mwambowu zili kumapeto.
Chikondwelerochi chichitikira ku likulu la wailesiyi ku Mangochi ndipo makwaya 19 atsimikiza kale kuti adzatenga nawo mbali
Wapampando wa komiti yoyendetsa mwambo wa chikondwelerochi a Andrew Chiromo atsimikimizira makwayawa kuti ayembekezere kudzakhala ndi chikondwelero chopambana kwambiri .
Iwo ati ngakhale chikondwelerochi simpikisano, makwaya omwe adzachite bwino adzalandira mphatso zosiyanasiyana pomwe mphatso yaikulu kwambiri ndi keyboard yapamwamba.
Mutu wachikondwalerochi chaka chino ndi Kufalitsa Uthenga wa Mulungu Mwa Njira Yatsopano, Potembenuka Mtima Moonadi Ndi Pochitira Umboni Chikhulupiriro Cha Chikhristu.
Chikondwelero cha mayimbidwechi chakhala chikuchitika kuyambira mu chaka cha 2004 ngati njira imodzi yokondwelera kubadwa kwa wailesiyi.