Akuluakulu a bungwe la utumiki wa apapa la Pontifical Missionary Societies PMS mmaiko a Britain ndi Ireland ayamikira akhristu a mpingo wakatolika mdziko muno kamba ka chidwi chawo pankhani zachipembedzo.
Mkulu wabungweli mdziko muno bambo Vincent Mwakhwawa ndi womwe anena izi polankhula ndi Radio Maria Malawi pamene alendowa akuyendera zitukuko zomwe bungwe lawo lakhala likuthandiza mudayosizi ya Zomba.
Bambo Mwakhwawa ati alendowa achita chidwi powona zitukuko zosiyanasiyana zomwe akhristu achita modzidalira komanso mothandizidwa.
Paulendowu alendowa ayamikiranso ana omwe akudzipereka kwathunthu mmabungwe a mumpingo.
Iwo apempha akatolika mdziko muno kuti atengere chitsanzo cha alendowa omwe akuti amapereka zochepa zomwe ali nazo pothandiza mpingo wa kuno ku Malawi.
Bungwe la utumiki wa apapa linakhazikitsidwa mdziko muno ndi cholinga chofuna kulimbikitsa akhristu kuti azikhala odzipereka potenga nawo mbali mu zochitika za mpingo.