Mpingo wakatolika mdziko la South Sudan wadzudzula achiwembu omwe apha meya wa mzinda wa Yei womwenso ndi likulu la dayosizi ya mpingowu mdzikolo.
Mai Cecelia Tito anasankhidwa kukhala meya wa mzindawo chaka chatha ,ndipo ati ndi mai woyamba kukhala paudindowu mumzindawo.
Iye anaphedwa limodzi ndi mmodzi mwa akuluakulu akuofesi yake kunja kwa mzinda wa Juba ndipo matupi a anthu awiriwa anapezeka pa 9 mwezi uno.
Mpingowu wati zomwe achiwembuwo anachita ndi kusokoneza ntchito zodzetsa mtendere mdzikolo, pamene malipoti ena akusonyeza kuti achiwembuwo ankafuna kuchita chiwembucho patchalitchi lina la mpingo wakatolika pomwe mayiyo ankatumikira.