Nduna ya zachitetezo mdziko la Ivory Coast a Paul Koffi Koffi alamula asilikali mdzikolo kuti abwelere mmalo awo ogwilira ntchito kamba koti achitapo kanthu pa zomwe asilikaliwo akudandaula.
Ndunayo yalamula asilikaliwo omwe dzulo anatseka misewu mmizinda iwiri kuphatikizapo mumzinda wa Abidjan omwe ndi likulu ladzikolo pokwiya ndi nkhani ya ndalama zapadera zomwe sakulandira.
Chiwonetsero chomwe asilikaliwo achita ndichoyamba chilowere paudindo pulezidenti Alassane Ouattara, yemwe adathetsa nkhondo yapachiweniweni yomwe inali mdzikolo mchaka cha 2011.
Anthu omwe athilirapo ndemanga pankhaniyi ati ichi ndi chizindikiro chakuti pang’ono ndi pang’ono anthu akutaya chikhulupiliro chawo mwa pulezidenti Ouattara pomwe chiwonetserocho chakhudzanso dera lomwe iye amakondedwa kwambiri.