Kwaya ya St Patricks yochokera ku Mangochi Cathedral mu dayosizi ya Mangochi, ndi yomwe yatenga chikho cha chaka chino cha chikondwerero cha mayimbidwe cha Radio Maria Malawi Choir Festival 2014.
Chikondwererochi chomwe chinachitika Loweruka pa 22 November 2014 ku likulu la wailesiyi m’boma la Mangochi, makwaya 19 a mpingo wakatolika ndi omwe analembetsa koma omwe anachita nawo chikondwelerochi ndi makwaya okwana 16.
Polankhula atangolandira chikhochi wapampando wa kwaya ya St Patricks a Arkangel Makhowi, anathokoza Mulungu chifukwa chomva pempho la kwayayi yomwe akuti yakhala ikulowa nawo pazikondwerero zotere kwa zaka zingapo koma siyimatenga chikho.
Iwo anati,“tili ndi chimwemwe chachikulu, tikumukweza ambuye kuti wayankha pemphero lathu.”
Pamenepa iwo alimbikitsa makwaya omwe zolinga zawo sizinakwaniritsidwe,kuti asafowoke pazikondwerero zomwe zikudza mtsogolomu.
“Cholinga chopitira ku mpikisano chimakhala chosiyanasiyana, timayenera kuzindikira chimene ifeyo tili. Ifeyo takhala tikulephera kangapo mu chikondwerero chimenechi, koma nthawi zonse tikabwerera timakakonza zolakwika zija,” anatero a Makhowi.
Mtsogoleri wa ma Judge pa chikondwelerochi a Felix Mtenthaonga ati atachita kawuniwuni anaona kuti nkoyenera kuti kwaya ya St Patricks itenge chikho kamba ka mmene anatambasulira mfundo zawo mu nyimbo yawo yopeka kudzera mu mutu wa chikondwererochi chaka chino zomwe makwaya ambiri zinawavuta.
Kwaya ya St.Peters Mkomeko yochokera ku dayosizi ya Dedza ndi yomwe yakhala nambala 2, kwaya ya St Lawrence Makankhula yochokera ku dayosizi yomweyo ya Dedza ndi yomwe yakhala nambala 3 ndipo pa nambala 4 pali Mtima Oyera Mitengo kwaya yochokera ku Archdayosizi ya Blantyre.
Chikondwerero cha mayimbidwe cha Radio Maria Malawi chimachitika chaka chili chonse ngati njira imodzi yokondwerera tsiku lomwe wailesiyi inakhazikitsidwa.