Bungwe lowona za chitukuko mumpingo wa katolika la Catholic Development Commission in Malawi (CADECOM) m`boma la Dedza lakhazikitsa ntchito ya zaka zitatu yotchedwa Zuze Intergrated Food Security pofuna kuthandiza alimi osauka kukhala odzidalira pachuma.
Mkulu wabungweli mudayosiziyo a Patrick Namakhoma ati ntchito imeneyi ithandiza kuchepetsa mavuto a chakudya kwa mabanja amene ali osowa kuti mabanjawa azipeza ndalama mosavuta.
Iwo ati cholinga cha ntchitoyo ndi kulimbikitsa ulimi wa mbewu komanso wa ziweto ngakhalenso ma banki a ku mudzi ndi cholinga chakuti anthu azitha kupanga ma bizinesi ang’onoang’ono.
Mwa zina,bungweli likhalanso likulimbikitsa ntchito yopereka madzi abwino komanso mbewu zamakono kwa alimiwa.