Bambo wina wa zaka 61 zakubadwa ali m’manja mwa apolisi m’boma la Neno kamba komuganizira kuti wapha m’bale wake pomuwombera ndi mfuti yochita kusema.
Ofalitsa nkhani za apolisi m’bomalo a Raphael Kaliati anauza Radio Maria Malawi kuti bamboyo yemwe dzina lake ndi Timothy Ephraim akumuganizira kuti anapha mdzukulu wake Christopher Patrick wa zaka 25 zakubadwa pa 21 mwezi uno.
Kaliati wati mnyamatayo anapita ndi mzake kukamwa mowa pa nyumba ya bamboyo pomwe anyamatawo anayamba kukangana.
Bamboyo ati anakatenga mfuti yomwe anasema ndi cholinga choti aletse mkanganowo ndipo malemuyo pofuna kulanda mfutiyo ndi cholinga choti bamboyo asachite nayo chipolowe, bamboyo anaomba mfutiyo pomwe chipolopolo chinakamenya mnyamatayo pa mtima ndipo anafera pomwepo.
Pamenepa a Kaliati anati apolisi atalandira uthengawu anathamanga pa malopo pomwe anapeza mnyamatayo atafa kamba koti anali ndi chilonda chachikulu pa mtima.
Iwo anati,“titafika pa malo a ngozi tinapeza mnyamatayo atamwalira kale ndipo thupi lake titalitengera ku chipatala, achipatala anatsimikiza za imfayi ndipo kuti anataya magazi ambiri.”
Malingana ndi a Kaliati a Christopher Patrick ankachokera mmudzi mwa a Matenda kwa mfumu yaikulu Mlauli, ndipo Timothy Ephraim amachokera mmudzi mwa Chidakwani mdera la mfumu yayikulu Chekucheku m’boma lomwelo la Neno ndipo akaonekera ku bwalo lamilandu ndikukayankha mulandu wakupha.