Bungwe la zachitukuko mu mpingo wakatolika la Cadecom mu Dayosizi ya Chikwawa lapempha mafumu onse opezeka mu dayosiziyo kuti achite zomwe angathe kuti ateteze anthu awo ku ngozi zogwa mwadzidzi zomwe zimakonda kuchitika mu nyengo ya mvula.
Mlembi wamkulu wa bungweli mu dayosiziyo a Reymond Kansale ndi amene anena izi pa mkumano wa mafumu umene bungweli lakhala likuchititsa mu diocese-yo.
A Kansale ati cholinga cha bungweli pokumana ndi mafumuwa chinali kufuna kuwazindikiritsa za udindo umene ali nawo poteteza anthu a m’madera mwawo kuti asamakhudzidwe ndi ngozi za kusefukira kwa madzi ndi zina zomwe zimachitika nthawi ya dzinja.
Iwo anati, “aliyense akuyenera kuzindikira kuti mavuto ogwa mwadzidzi amadza kamba ka kusintha kwa nyengo, bungwe lathu likufuna kupeza njira zochepetsera mavuto ngati amenewa.”
A Kansale anapitiriza kufotokoza kuti anthu amene amakhala malo amene ali pa chiwopsezo cha ngozi zogwa mwa dzidzidzi akuyenera kusamuka.
Bungwe la Cadecom likugwira ntchitoyi pofuna kuchepetsa mavuto amene amadza nthawi ya nyengo ya dzinja.