Nthumwi zoyimilira mabungwe a utumiki wa a papa la Pontifical Missionary Soceties (PMS) zochokera m’mayiko a Ireland ndi England zati zakhutira ndi momwe mpingo wakatolika mu Diocese ya Zomba ikugwilira ntchito zake.
M’thumwizi zomwe zinalipo zinayi, zinafika m’dziko muno pa 15 mwezi uno ndipo mwa zina, zakhala zikuyendera zitukuko zosiyanasiyana zomwe zakhala zikuchitika ndithandizo lochokera kwa mamembala abungweli m’mayiko awiriwa.
Mthumwizi zayamikiranso chidwi chimene akhristu ampingo wakatolika akhala akuonetsa pogwira ntchito zokometsa miyambo ya chipembedzo.
M’modzi mwa alendowa Mayi Shillar Isaac ati ndiwokondwa ndi momwe akhristu a mpingo wakatolika mu diocese ya Zomba akhala akuwasamalira m’masiku khumi amene akhala ali m’dziko muno.
Iwo ati,“izi zasonyezelatu kuti anthu amdziko muno ndinu anthu odziwa kulandira bwino alendo.”
Mayi Isaac atsindika kuti akabwelera akapitiliza kuthandiza mpingo wakatolika mdziko la Malawi kuti umodzi umene Ambuye Yesu Khristu amatiphunzitsa upitilire kufalikira pakati pathu.
Mkulu wa bungwe la utumiki wa apapa m’dziko muno bambo Vincent Mwakhwawa omwe akhala akuyenda limodzi ndi alendo wati ndi wokondwa kuti kufika kwa alendowa kwathandizanso kuzindikiritsa akhristu kudziwa zaudindo umene ali nawo pothandiza mpingo modzipeleka monga momwe akhristu aku Ireland ndi England akuchitira.
“Ife ampingo wakatolika mdziko muno taphunzira zambiri monga kukhala wokhwima maka pogawana ndi anzathu zomwe tili nazo komanso chikondi pakati pathu,”anatero bambo Mwakhwawa.
Bungweli linakhazikitsidwa mmayiko osiyanasiyana ndi cholinga chofuna kulimbikitsa mtima wautumiki, umishonale, wokonda mpingo ndikuwuthandiza.