Boma lati lili ndi chikhulupiriro chakuti mdziko muno muli miyala yambiri ya mtengo wapatali yomwe ingathe kugwiritsidwa ntchito potukulira chuma cha dziko lino.
Wachiwiri kwa mkulu wowona zachilengedwe chapansi pa nthaka mu dipatimenti yowona zakafufuku ya Geological Survey a Joefu Salima, ndiwo anena izi lamulungu pa 23 November m’boma la Mangochi pamsonkhano ozindikiritsa anthu zomwe boma likuchita pofuna kuyambitsa ntchito zamigodi mdziko muno.
A Salima ati pafupifupi mayiko onse omwe achita malire ndi dziko lino ali ndi migodi yosiyanasiyana zomwe zikupereka chitsimikizo ku boma choti mdziko munonso mukhoza kukhala miyala yomwe ikupezeka mmaiko oyandikana nawowa.
“Tili ndi chikhulupiliro kuti miyala imene ikupezeka mmayiko oyandikana nawo kunonso iliko, chomwe chikufunika ndi chakuti amalawi azindikire ntchitoyi ndi cholinga chakuti ayitsatire bwino,”anatero a Salima
Iwo ati bungweli linachita kale kafukufuku wamiyala imene ili mdziko la Malawi yomwe ingathe kutukula dziko lino.
Zotsatira zomwe zikuyembekezereka kutuluka mwezi wa January kapena February zikatuluka, adzayitana anthu a mdziko muno ngakhale akunja amene angathe kuchita bizinesi ndi dziko lino.