Msonkhano wa mabungwe ang’onoang’ono a mumpingo wakatolika omwe wakonzedwa ndi mabungwe a ma episkopi mmayiko a Madagascar ndi Africa uli m’kati mdziko la Ghana.
Zina mwa mfundo zomwe nthumwi ku msonkhanowo zikuwunika momwe mpingowu ungayendetsere chaka cha chiyanjano cha mayiko a mu Africa chomwe mtsogoleri wakale wampingo wakatolika padziko lonse Papa Benedikito wa 16 opuma, adanena kuti mayikowa aziganizira.
Nthumwi kumsonkhanowo ndi zochokera mmabungwe osiyanasiyana a mumpingowu muno mu Africa,omwe ndikuphatikizapo ochokera m’bungwe la Amecea.
Msonkhanowu ukuchitika potsatira msonkhano wina okambirana zomwe mabungwe ang’anoang’ono mumpingo angachite pofuna kudzetsa umodzi pakati pa anthu mmayiko a muno mu Africa omwe udachitikira ku Nairobi mdziko la Kenya.
Papa Benedikito wa 16 opuma adapempha kuti dziko lililonse la mu Africa chaka ndi chaka liziyika padera tsiku kapena sabata imodzi maka mu nyengo yoganizira kubadwa kwa Yesu Khristu kapena ya masautso ake polimbikitsa chiyanjano pakati pa anthu kulikonse komwe akukhala.