Ana atatu a banja limodzi amwalira m’boma la Ntchisi ndipo anthu ena 16, awagoneka pa chipatala cha boma m’bomalo atadya chakudya chomwe akuchiganizira kuti chinali ndi poyizoni.
M’neneri wa apolisi m’bomalo Sergeant Gladson M’bumpha watsimikiza za nkhaniyi ndipo wati ana omwalirawo ndi Yohane Davison wa zaka khumi ndi ziwiri zakubadwa, Labani Raphael wa zaka zisanu ndi chimodzi , komanso Evason Raphael wa zaka khumi ndi ziwiri a m’mudzi mwa Kaphuka m’dera la mfumu yaikulu Nthondo m’boma la Ntchisi
A M’bumpha ati loweruka lapitali madzulo, anthuwo anayamba kusanza komanso kutsekula mmimba atadya nsima yomwe ndiwo zake zinali nyemba zomwe adazitenga kwa achibale awo komwe anthu awiri a pa mudziwo adapita kukacheza kwa tsiku limodzi.
Pofika lolemba sabata ino anthuwo anapita kuchipatala kuti akalandire thandizo, komwe anawo amwalirira.
M’modzi mwa anawo wamwalira lolemba cha mma 10 koloko usiku motsatizidwa ndi wina ndipo wachitatu wamwalira lachiwiri mmawa.