Nthambi zowona ubale wa mipingo ndi zipembedzo kulikulu la mpingo wakatolika komanso kuchisilamu, zadzudzula magulu osiyanasiyana omwe akuchitira anthu zamtopola mudzina la chipembedzo.
Magulu awiriwa adzudzula mchitidwewu kudzera mchikalata chomwe atulutsa,pambuyo pamsonkhano wamasiku awiri womwe anali nawo mumzinda wa Tehran mdziko la Iran.
Iwo atsindika kuti kukambirana pamene pali kusamvana pakati pa anthu a zipembedzo zosiyana nkofunikira kwambiri pofuna kuwonetsetsa kuti anthu akukhala mwa bata ndi mtendere.
Chikalatacho chapempha nyumba zofalitsa nkhani kuti zidzipereke pofalitsa nkhani zomwe zingamange ubale wabwino pakati pa akhrisitu ndi asilamu omwe mmayiko ena sakutha kukhala mwamtendere chifukwa chosiyana chipembedzo.