Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Nkhanza za Mbanja Zikukolezera Kufala kwa Matenda a Edzi

$
0
0

Bungwe la Southern Africa Aids Trust SAAT lati nkhanza za m’banja ndi vuto limodzi lomwe likukolezera kufala kwa kachilombo ka HIV komwe kamayambitsa matenda a Edzi.

Mkulu wabungweli a Robert Mangwazu Phiri ndi yemwe wanena izi polankhula ndi Radio Maria Malawi.

A Mangwazu Phiri anena izi pamene mayiko padziko lonse kuyambira pa 25 November mpaka pa 11 December akuganizira za nkhanza za m’banja zomwe zikubwezeretsa ntchito mmbuyo zosiyanasiyana kuphatikizapo zachitukuko.

Iwo apempha mabungwe osiyanasiyana kuphatikizapo omwe siaboma,kuti adzipereke pofuna kuti limodzi ndi bungwe la SAAT alimbane mokwanira ndi matendawa.

“Tikufuna mabungwe ena kuti tigwirane nawo manja kamba koti matenda a Edzi amakhudza mbali zosiyanasiyana,”anatero a Phiri.

Bungwe la SAAT likugwira ntchito mmadera a mmidzi ndi mafumu ndi cholinga chofuna kuti vutoli likhale likuchepa.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Trending Articles



<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>