Episkopi wa Arch dayosizi ya Lilongwe ya mpingo wakatolika Ambuye Tarsizius Ziyaye walimbikitsa ma membala a bungwe la Legio kuti apitilize kudzipereka pogwira ntchito zawo mu mpingo.
Ambuye Ziyaye amalankhula izi loweruka ku Maula Cathedral mu mzinda wa Lilongwe pomwe amakhazikitsa Sinatusi ya Legio ya Maria ku parish ya Maula mu dayosiziyo.
Iwo ati bungweli limathandiza kukokera nkhosa zofowoka ku chipulumutso kudzera mwa Amayi Maria.
Ambuye Ziyaye ati,“tikamapemphera mu uneneri wa Amayi Maria, mapemphero athu amamveka ndipo tikamalemekeza amayiwa, tiwalemekeze mowonadi.”
Polankhula pa mwambowu mkulu woyang’anira mabungwe a mu mpingo mdziko muno BamboVincent Mwakhwawa wati kukhazikitsa kwa Sinatusi mu dayosiziyo zasonyeza kuti ntchito za bungweli zikupita patsogolo.
“Ine chimwemwe changa ndi chachikulu kamba koti tapatsidwa mphamvu kuchokera ku likulu la bungweli ku Dublin kuti tiyang’anire ma dayosizi atatu mdziko muno omwe ndi Karonga, Mzuzu komanso Dedza,”anatero Bambo Mwakhwawa.
Pulezidenti wa bungwe la Legio ku Maula Cathedral mayi Elizabeth Kamoto anati ndi wokondwa kuti akwezedwa kukhala Sinatusi ndipo ati adzipereka pa ntchito zokweza bungweli potsata malamulo a Legio.
Sinatusi ndi likulu la Legio ya Maria yomwe imakhazikitsidwa ndi likulu la Legio pa dziko lonse lapansi kuchokera ku Dublin.