Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Sukulu ya Ukachenjede ya DMI Itengapo Mbali Pokweza Maphunziro a Ana

$
0
0

Ena mwa mabungwe omwe siaboma m’boma la Mangochi ayamikira sukulu ya ukachenjede ya St.John The Batist, DMI,kamba koyikanso chidwi pantchito zosula ana msukulu za pulayimale m’bomalo.

Mkulu wabungwe la SEED Malawi a Agly Mfune ndi yemwe walankhula izi pamwambo okumbukira tsiku la ana padziko lonse omwe unachitikira pasukuluyi loweruka m’boma la Mangochi.

A Mfune omwe analinso mlendo olemekezeka pamwambowu, ati ali ndi chikhulupiliro chakuti pakutha pa zaka zinayi mbiri ya boma la Mangochi pankhani yotsalira pamaphunziro isintha kamba ka luntha lapadera lomwe asisiteri omwe amayendetsa sukuluyi ali nalo pantchito yotukula amai ndi ana.

Pamenepa a Mfune anatinso nkhanza za mbanja ndi ena mwa mavuto amene  amabwezeretsa mmbuyo maphunziro a ana.

Iwo anati, “kale timati mwana amachitiridwa nkhanza ndi munthu wosamudziwa, koma pano zikuwonekera poyera kuti ana mmabanja sakutetezedwa.”

Mwa zina sukulu ya ukachenjede ya DMI inakhazikitsa nyumba yamalamulo ya ana,yomwe pakadali pano ili ndi ophunzira 750 ochokera Boma la Mangochi.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>