Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

PAPA APEMPHA MAPEMPHERO KWA AKHRISITU

$
0
0

Mtsogoleri wa Mpingo wa katolika pa dziko lonse Papa Benedikito wachi 16 wapempha akhrisitu kuti amupempherere pamodzi ndi Papa yemwe adzalowe m’malo mwake mtsogolomu.

Papayu walankhula izi  kwa akhrisitu amene anasonkhana kulikulu la Mpingowu ku Vatikani pamwambo wa sabata iliyonse womwe amalankhula kwa anthu.

Aka kanali koyamba kuti Papa Benedikito wachi 16 awonekere kwa anthu chilengezereni kuti adzapuma pa udindowu pa 28 mwezi uno.

M’mawu ake kwa akhrisitu zikwizikwi omwe anasonkhana ku malowo, mtsogoleri wa Mpingo wa katolikayu wati waganiza zopuma pa udindowu mwa ufulu komanso moganizira Mpingowu pambuyo popemphera kwa nthawi yayitali kwa Mulungu.

Papayu wathokoza anthu onse chifukwa chomuwonetsera chikondi komanso ku mupempherera ndipo wapempha akhristu kuti apitirize kupempherera mpingowu.

 

 


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>