Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

MPINGO WA KATOLIKA KOMANSO ANGILIKANI ALOWA M'NYENGO YA LENT

$
0
0

 

Akhrisitu a Mpingo wa Katolika komanso Angilikani pa dziko lonse  lapansi ayamba nyengo yokumbukira masautso a Yesu Khrisitu.

Nyengoyi imayamba ndi mwambo wa nsembe ya misa ya phulusa, pomwe akhrisitu amalembedwa chizindikiro cha mtanda pa mphumi pofuna kulimbikitsidwa kulapa machimo awo kuti ayanjanenso ndi Mulungu.

Nyengoyi yomwe imakhalapo chaka ndi chaka, imachitika kwa masiku makumi anayi  pomwe akhrisitu amapemphedwa  kulapa machimo awo, kudzilanga komanso kusala zinthu zosiyanasiyana zomwe iwo amakonda m’moyo wawo watsiku ndi tsiku.

Nyengoyi imatha lachisanu loyera pomwe akhrisitu amatsendera chikumbutso cha masautso a Yesu khrisitu pa njira ya mtanda yomwe amachita pa m’dipiti kunja  kwa matchalitchi awo.

Pamene nyengoyi yayamba akhristu amapemphedwanso kusonkhana m’matchalitchi awo pamwambo wa njira yamtanda lachisanu lililonse, kufikira lachisanu loyera-lo lomwe chaka chino likhale pa 29 March.

 

 


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Trending Articles


Mdima unadetsa dziko



<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>